Wednesday 23 January 2013

MA YOUTH CAMPS KU MPOTO



ZOTSATIRA ZA ZOKAMBIRANA ZOKHUDZA MA YOUTH CAMPS KU MPOTO 



DATE: 19 JANUARY 2013 

Pemphero lotsekulira:                          Deacon Luwanda    (Dunduzu)

Kupereka mbiri ya zokambirana zakale. (recap)

Malingana ndikuti ma secretary onse awiri sanabwere ku zokambiranazi wapampando wa komitiyi Frighton Kachule ndi amene anapereka mbiriyi m`malo mwake. Cholinga cha mbiri chinali kukumbutsana zomwe anakambirana kale, komanso kufuna kudziwa zomwe zinakwaniritsidwa ndi zomwe zikufunika kuchitika.

Mbiri ya zachuma

Atatha chairman kupereka lipotili naye msungichuma anapereka lipoti lake la za chuma: Iye mu lipoti lake anati ndalama zonse zinali 4000 kwacha koma pamene tinakumana pa tsikuli tinagwiritsa tchito ndalama zokwana 1.160 kwacha zomwe tinagulira chakudya ndipo pakali pano kuthumba kwathu kwatsala ndalama zokwana 2,840 kwacha. Ndalamazi sizikukwana kuyendetsera bungwe la chinyamata pa regional level kotero chinyamata chathu chikuyenera kupeza njira zomwe zingathandize kukweza chuma chathu. (fumbi ndiwe mwini)

Mfundo zomwe zinakambidwa:

  1.     Kalata yochokera ku Luwazi joint 
  2.     Malo eni eni ochitirapo half ndi full camp 
  3.     Kukonza masiku a ma youth camps 
  4.     Camp fee 
  5.     Kukonza dongosolo la kasonkhedwe ka zakudya za pa half camp 
  6.     Malamulo apa camp 
  7.    Mbiri (report) yochokera ku National Youth Committee


MUTU OYAMBA:

KALATA YOCHOKERA KU LUWAZI JOINT
Itafika nthawi yolandira nfundo zoti tikambirane kuchokera kwa nthumwi za komiti, Luwazi joint kudzera mwa chairman wawo Charles Mkandawire inapereka kalata yawo yomwe inali yodandaula kuti iwo akufuna full camp osati half camp monga momwe zinakhalira. Ndipo chairman wakomitiyi Frighton Kachule anawerenga kalatayo pamanso pa anthu onse yomwe inali motere:


Luwazi Y Joint
Prvate Bag 63
Mzuzu

5th January 2013
The chairman
Northern Youth Association Committee
Mzuzu

Mutu: Kalata wokhudza youth camp

Takhala pansi ndikugwirizana kuti ife tikupempha full camp osati half camp pa zifukwa izi:
         i.            Ife kuno takhalitsa osakhala ndi full camp
        ii.           Ife timaziwa kuti timayendera circle pokonza camp osati chisawawa
      iii.           Ifeyo tayenda kwambiri kwa anzathu
Ngati zingalephere kutipatsa full camp ndiye tikupempha kuti ndibwino kuti nayo half camp yomwe munatipatsa ipite kaye kwa ena, kaamba koti ifeyo sitili okonzeka kukhala ndi half camp ndipo tidzadikira mpaka chaka chomwe mudzatipatsire full camp. Komabe izi sizikusonyeza kuti tiri okhumudwa ayi, ife tili okonzeka kupita kulikonse komwe kungakhale camp.
M`malo mwa komiti yonse ya Luwazi Youth Joint, ine wanu mwa mbuye:
                                                                                                 
Michael Mtepa                                                                                         Charles Mkandawire
(Secretary)                                                                                                                     (Chairman )

Pakukambirana za nkhaniyi, komiti inawona kuti kunali kofunika kuwathandiza pa pempho lawo pa zifukwa zomwe anenazo komanso panali zifukwa  zina zowonjezera pamenepa monga:
·         Pali chikayiko ngati a Lusimbo angakwanitse kukonzekera full camp
·         Nthawi zambiri achinyamata aku Lusimbo sawonetsa chidwi cheni cheni pakusonkhana ndi anzawo.
·       Malo komanso zinthu zokonzekera msonkhano ndizosadalirika ku Lusimbo kufikira akulu akulu association atayenderako kaye

Pazifukwa zonsezi, pomaliza komiti inagwirizana kuti tsopano Half camp ipite ku Lusimbo ndipo Full camp ipite ku Luwazi

Koma komitiyi inatsutsa nfundo nambala 2 ya mkalata wa Luwazi yomwe imanena kuti iwo amadziwa kuti pokonza misonkhano ya camp zimayendera circle osati chisawawa. Pamenpa chairman anafotokoza kuti 1). Ganizo loyika msonkhano umodzi ku Henga joint linabwera pofuna kuwaganizira achinyamata a Henga joint pankhani ya transport kuti asayende ma ulendo awiri atali atali okha okha chaka chino chokha malingana ndi kukwera mitengo ya ma transport. 2).  Ndizoona kuti mwadongosolo camp ina imayenera ku chitira ku Mzuzu koma Kaamba koti a Mzuzu joint akhala otanganidwa ndi msonkhano wa ukulu wa zimayi chaka chino ndiye kukhala kovuta kuti akonzekerenso camp. Ndichifukwa chake zawoneka ngati kuti sitinayendere circle posankha malo ochitira ma-camp. 

Langizo kwa onse: 
Komabe ndi bwino kuti tisamakhale ndi chizolowezi chakuti zinthu zimayenda chonchi ayi, zinthu zimasintha malingana ndi nyengo yake. Tisamayiwale kuti chizolowezi nthawi zonse chimawononga zinthu.

Phunziro lomwe tingapeze mu nkhaniyi: 
Tikuyamikira kwambiri njira imene Luwazi joint inagwiritsa tchito pofuna kuthetsa vuto lomwe analiwona. Njirayi ikupereka ulemu kwa komityi ndi  nthumwi zonse pozindikira kuti amataya ndalama komanso nthawi pofuna kuti akambirane zinthu ngati zimenezi ndi chifukwa chake sanafune kuti zingothera pafoni kapena kumangoveketsa nkhani zamabodza zomwe sindizo. Ndibwino kuti titengerepo phunziro kuti ngati pali nkhani yomwe sinakusangalatseni kapena mwafuna kuti pena pake pa sinthidwe ndibwino kulemba kalata kapena kutumiza nthumwi yanu ku zokambirana za association kuti nkhaniyo ikakambidwe pa komiti osati kumangoyamba kufalitsa mabodza kapena pafoni ayi. Zindikirani kuti a Luwazi joint sanachiyesere chamwayi kuti poti chairman ndi wa ku joint kwawo ndiye angopanga zomwe akufuna ayi komanso naye chairman sanatengere kuti poti ndi anthu a joint yake ndiye angosintha zinthu popanda kudzera kukomiti ayi. Dziwani kuti chairman siwa joint imodzi ayi ndipo sayimira mbali ayi. Tiyeni tiziyendetsa zinthu mudongosolo kuti chinyamata chathu chikhale chopambana.

MUTU WA CHIWIRI: 

MALO ENI ENI OCHITIRA MISONKHANO YA CAMP
Malo ochitira misonkhano ya youth camp ndi Lusimbo yomwe ndi Henga joint ndi  Luwazi komwenso ndi Luwazi joint. Malingana ndi zokambirana za pa 24 Novermber 2012 komiti inawunika zina mwa fundo zomwe zimapangitsa kuti kafalitsidwe ka uthenga wabwino kasapite pa tsogolo mu mpingo mwathu komwe tinapeza kuti kuphatikiza kuti tilibe njira zamphanvu zofalitsara uthenga wa Mulungu, tikamachita misonkhano yathu timachitira malo amodzi modzi chaka ndi chaka monga pa tchalitchi zomwe zimapangitsa kuti tisamafikire anthu omwe akusowekera uthengawu. Pa chifukwa cha ichi komiti inagwirizana kuti tsopano tiyense kumapangira  misonkhano ya youth camp kutali ndi ma tchalitchi, ndicholinga choti tikafikirenso anthu ena achilendo komanso ngati njiri imodzi yofalitsira mbiri ya mpingo wathu kuti uzidziwika ku madera ambiri adziko lino. Kotero tinawapempha ma joint onse amene kukachitikire camp kuti akafune malowa kutali ndi ma tchalitchi awo:

Ku Lusimbo, Half camp ikuyenera kukachitikira pa Chichi primary school pamene ku Luwazi full camp ikuyenera kudzachitikira pa Mwambazi primary school koma ngati pangakhale kusintha tidzadziwitsidwa nthawi ya camp isanafike:   

    
Malo a Half Camp 2013
Henga Joint (Rumphi)        >     Lusimbo SDB Church     >       Chichi  Primary School 

     
            Malo a Full camp 2013

Luwazi Joint (Nkhata Bay)      >      Luwazi SDB Church     >    Mwambazi  Primary School
               
MUTU WACHITATU: 
KUKONZA MASIKU OCHITIRA MISONKHANO YA YOUTH CAMP

Half camp

APRIL       2013
S          M        T         W        T         F          S
            1          2          3          4          5          6
7          8          9          {10       11        12        13}
14        15        16        17        18        19        20
21        22        23        24        25        26        27
28        29        30

Idzayamba pa Wednesday, 10 April mpaka pa Saturday (Sabbath)  13 April 2013  (masiku atatu)


Full camp

AUGUST      2013
S          M        T         W        T         F          S
                                                1          2          3
4          5          6          7          8          9          10
{11       12        13        14        15        16        17}
18        19        20        21        22        23        24
25        26        27        28        29        30        31


 
 Idzayamba pa Sunday, 11 August mpaka pa Saturday (Sabbath) 17 August 2013 (masiku 7)

   
Masikuwa anakonzedwa malingana ndi kalindala ya ma sukulu onse dziko muno yomwe ili motere
Term
Tsiku lotsekulira
Tsiku lotsekera
Utali wa nyengo ya Masiku a tchuthi
Masabata a tchuthi
Yoyamba
3 March 2012
7 December 2012
7 December 2013 mpaka pa 6 January 2013
Anayi     (4 weeks)
Yachiwiri
7 January 2013
22 March 2013
22 March  mpaka pa  21 April 2013
Anayi     (4 weeks)
Yachitatu
22 April 2013
26 July 2013
26  July mpaka pa 1 September 2013
Asanu    (5 weeks)

MUTU WACHINAYI:

CAMP FEE
Fundoyi inaperekedwa ndicholinga chofuna kuwunikanso zaubwino omasonkha camp fee komanso kuyipa kwake ngati kulipo. Ngakhale kuti ndi chachilendo mu mbiri ya chinyamata kuno ku mpoto ndi kutinso anthu sanazolowere kusonkha camp fee Komabe anthu ambiri akuyamikira kuti camp fee ikumathandiza kwambiri maka maka pamene tili pa camp, chitsanzo camp imene tinali nayo ku Echizweni, malingana ndi kuchepa kwa zakudya msonkhano unayenera kuthera panjira koma camp fee inatithandiza kugula zakudya mpaka tinamaliza msonkhano kuphatikiza pamenepa timagulira mankhwala omwe amatithandizanso kwambiri pa nthawi yomwe tili pamsonkhano. Pachifukwa cha ichi panali ganizo loti mwina achinyamata asiye kumasonkha zakudya popita ku camp m`malo mwake tingokweza camp fee, mu m`kukambirana mthumwi zinawona kuti sikwabwino kuti tingokwezeratu camp fee ndi kuchotsa zakudya zomwe achinyamata amanyamula kaamba koti kudyamula kwa zakudya kumathandiza kuchepetsa ndalama zomwe anyamata amawononga pokonzekera youth camp komanso kukweza kwa camp fee kudzapangitsa kuti anthu ena ovutika komanso achichepere alephere kupita ku camp.  Komabe malingana ndi kukwera kwa mitengo ya zinthu m`dziko muno K250 yomwe timasonkha ngati camp fee sikukwanira ayi kotero tinagwiri zana kuti camp fee tsopano ikhale K500 aliyense koma tachotsako zakudya zina zomwe timanyamula monga: zomwela tea, mafuta ophikira, mchere, masamba a tea ndi sugar, m`malo mwake achinymata azingonyamula ufa ndi ndiwo basi

>>Camp fee:               K500              Aliyense                 

Akulu akulu (am`khala pakati) komanso aziphunzitsi onse akuyenera kudzanyamula camp fee pobwera ku camp, koma sakuyenera kusonkha nawo zakudya komaso transport ikuyenera kukonzedwa ndi achinyamata omwe akuyenda nawo.



MUTU WACHISANU:                
 DONGOSOLO LA KASONKHEDWE KA ZAKUDYA ZA HALF CAMP

Henga Joint
Tikuyembekezera Anthu osachepera
Ufa
Ndiwo / Ndalama
Khanga + Phompha
15
Mathini Atatu    (3)
10 kg Nyemba kapena ndalama K2000
Mzale
30
Ma thini     6
20 kg Nyemba kapena ndalama K4000
Lusimbo
15
Mathini Atatu     (3)
10 kg Nyemba kapena ndalama K2000
Uzumala + Sasi
10
Mathini  awiri     (2)
10 kg Nyemba  kapena ndalama K 1500

Luwazi Joint
Tikuyembekezera Anthu osachepera
Ufa
Ndiwo / Ndalama
Majiga + Chinguluwe
3
Thini Lomodzi    (1)
5 kg Nyemba kapena ndalama K1000
Lisale + Manyenyezi
15
Mathini Anayi   (3)
10 kg Nyemba kapena ndalama K2000
Luwazi
20
Mathini Atatu   ( 4)
15 kg Nyemba kapena ndalama K3000

Mzuzu Joint
Tikuyembekezera Anthu osachepera
Ufa
Ndiwo / Ndalama
Dunduzu
30
Ma thini    6
20 kg Nyemba kapena ndalama K4000
Jandalala
12
Mathini awiri    ( 2)
10 kg Nyemba kapena ndalama K2000
Mchengautuwa
10
Mathini Atatu     (2)
10 kg Nyemba kapena ndalama K1500
Zolozolo
10
Mathini  awiri     (2)
10 kg Nyemba  kapena ndalama K1500

Zindikirani kuti pa anthu asanu  aliwonse pakuyenera pakhale thini limodzi la ufa komanso 5kg nyemba kotero chiwerengero chikakwera ndi anthu 5 aliwonse mukuyeneranso kuwonjezera kuchuluka kwa chakudya chanu malingana ndi mulingo omwe waikidwawu. Kumbukiraninso kuti dongosolo la chakudya ichi ndi la  pa Half camp basi,  ya full camp ikonzedwabe kutsogolo kuno.


MUTU WACHISANU NCHIMODZI: 

MALAMULO APA CAMP

Pofuna kuchepetsa zibwana zomwe zimachitika ku camp, komiti inawona kuti ndikofunikira kuti pakhale malamulo omwe aliyense wopita ku camp akuyenera kuwatsatira. Ndipo malamulo amenewa akuyenera kugwira ntchito kwa wina aliyense posatengera komwe akuchokera, maonekedwe, kukula kapenanso udindo omwe alinawo. Ndipo ndi cholinga cha komitiyi kudziwitsiratu achimata komanso anthu onse ofuna kudzakhala nawo pa ma camp anthu kuti adziwiretu malamulo amenewa ndipo yense obwera ku camp kusonyeza kuti akugwirizana nawo malamulowa ndikuti akuyenera kutsatira zonse.
Ndipo malamulowo ali otere:

YENSE WOPHWANYA MALAMULO OTSATIRAWA PA CAMP AKUYENERA KUBWEZEDWA
1)  Aliyense akuyenera kupezeka pa camp nthawi iliyonse kuyambira tsiku lofikira mpaka lomaliza
                                                               i.      Ngali ali ndi zochitazina ndi bwino akachite asanafike pa camp kapena itatha camp       
2)    Aliyense akuyenera kupezeka pakalasi panthawi ya mphunziro
3)  Ikakwana nthawi yogonera aliyense akuyenera kukagona pamodzi ndi amnzake onse
                                                               i.      Pasapezeke wina palibe pa nthawi yogona kumalo komwe wapatsidwa kugona ndi amnzake
4)      Sipadzapezeka munthu opita kogona thawi isanakwane
                                                               i.      Ofuna kugona pazifukwa zina monga kudwala akuyenera kugona pomwe pali amnzake kapena pa kalasi pomwepo kufikira nthawi yokagona itakwana
5)      Munthu asayende mopitilira malire omwe ayikidwa pa camp
6)      Aliyense akuyenera kuvala modzilemekeza
                                                               i.      Sibwino kuvala zovala, zothina, zominula, zowonekera mkati, zikuku zikulu (over size) kukhwefula, ma tcheni, zibangiri, nyotsonyotso ndi zina zambiri.
7)      Nthawi ya chakudya ikhale imodzi, chakudyanso chimodzi
                                                               i.      Ndibwino kuwonetsetsa kuti zipangizo zolandilira zakudya zilipo tikamayandikira kulandila chakudya
                                                              ii.      Pasapezeke munthu akumachedwa ndi kuchita zina panthawi ya chakudya
8)      Asachoke munthu pa camp ndikuyendera zinthu zina osati za pa camp
                                                               i.      Ngati munthu ali ndi zochita zina, monga, kutumidwa ndi makolo kapena kukawona abale ndi bwino kuti azichitiratu izi asanafike ku camp kapena itatha camp, chifukwa zimenezi zimasokoneza chitetezo cha pa camp.
9)      Malo ogona akhale amodzi malingana ndi gulu lomwe munhtu wapatsidwa
                                                               i.      Asapezeke munthu akukagona kunyumba kapena kwina kwake kuleka malo omwe wapatsidwa pa camp-po
10)    Nthawi yosamba ikhale imodzi
                                                               i.      Asapezeke munthu akupita kukasamba nthawi ya zochitika zina: monga (nthawi ya phunziro kapena kudya ndibwino kuti awonetsetse ngati akuchita zimenezi asasoneze zochitika zina)
                                                              ii.      Asapezeke munthu akupita kukasamba kwina kusiya malo omwe wapatsidwa pa camp- po (chifukwa zimasokoneza dongosolo la kasambidwe komanso limayambitsa chisokonekero popeza aliyense amakasamba komwe wafuna)
11) Gulu la chinyamata lililonse lizipita ndi am`khala pakati akulu akulu m`modzi kapena awiri popita ku camp
                                                               i.      Am`khala pakatiwa akhoza kukhala akulu ampingo ( ma dkioni ) kapena munthu aliyense koma wamkulu yemwe angathe kulangiza bwino achinyamata.
1.         Akuyeneranso kukhala amayi womwe angalangize bwino atsikana komanso m`bambo amene angatsogolere achinyamata bwino.
12) Gulu lililonse la chinyamata likuyenera kunyamula chakudya chokwanira monga      momwe dongosolo likunenera
                                                               i.      Gulu lomwe lidzanyamule chakudya choperewera likuyenera:
1.         Kulipitsidwa chindapusa choyelekeza chakudya chomwe chapereweracho kapena
2.       Kubwezedwa kufikira  atakonzeka bwino
Chifukwa kubwera ndi chakudya choperewere pa camp kumabweretsa mavuto monga:
·         Mapokoso kwa omwe abweretsa chakudya chokwana                         komanso
·         Kuperewera kwa chakudya pa camp zomwe zimazunzitsa anthu osalakwa
·         Kuwonongeka kwa ndalama zambiri zomwe zikanagwira ntchito zina



MUTU WACHISANU NCHIWIRI:

MBIRI (REPORT) YOCHOKERA KU NATIONAL YOUTH COMMITTEE

Chairman anapereka zotsatira za zokambirana za Malawi youth committee yomwe inachitikira ku Lilongwe pa 8 December 2012.
Ndipo zina za izo kunali ku sankhanso komiti yatsopano imene idziyendetsa chinyamata Malawi yonse ndipo inali motere:

Chairman                               :               Maxwell Maida                        (Lilongwe)
V chairman                            :               Malumbo Mkandawire             (Blantyre)
Secretary                               :               Hannah Ganunga                      (Lilongwe)
V-Secretary                           :               Chancy Mbewe                        (Thyolo)
Treasure                                :                    Peter Mbite                              (Thyolo)
Activity Coordinator             :               Tennis Molande                        (Lilongwe)
Committee members
           :               Billy Sokole                             (Mzuzu)
           :               Frighton Kachule                    Nkhata Bay
           :               Central Region Chairman      (……………..)
           :               Southern Region Chairman   (………………)

Unform:  
National committee inakhazikitsa uniform  yomwe mtundu wake ndi navy blue pansi ndi white m`mwamba ndipo ma chairman onse a joint anapatsidwa zitsanzo za msalu zimenzi, ndipo aliyense ofuna kukagula msaluzi akuyenera kufotokozera chairman kuti amupatse chitsanzo ndi cholinga choti isakasiyane posankha: Mukafuna kudziwa zambiri funsani a chairman a joint yanu kuti akufotokozereni bwino kapena mungathe kuimba foni kwa chairman wa association pa 0888725175. Ndipo munthu akafuna kusoketsa suti, yonse idzikhala ya navy blue pansi ndi m`mwamba momwe.                                 Msapato zakuda
Ndipo aliyense akupemphedwa kuti akhale atagula unformyi potha pa chaka chino
Pemphero lomaliza:               Mr Mbewe               (Dunduzu)